feet

Uthenga Wabwino wa Yohane

A True Story



Mawu Asandulika Thupi

1Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu ndiye Mulungu. 2Mawuwa anali ndi Mulungu pachiyambi. 3Zinthu zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo popanda Iye sikukanakhala kanthu kalikonse kolengedwa. 4Mwa Iye munali moyo, ndipo moyowo unali kuwunika kwa anthu. 5Kuwunika kunawala mu mdima, koma mdimawo sunakuzindikire. 6Kunabwera munthu amene anatumizidwa kuchokera kwa Mulungu; Iyeyo dzina lake linali Yohane. 7Iye anabwera ngati mboni kudzachitira umboni kuwunikako kuti kudzera mwa iye anthu onse akhulupirire. 8Iyeyu sanali kuwunika; koma anabwera ngati mboni ya kuwunika. 9Kuwunika koona kumene kuwunikira munthu aliyense kunabwera ku dziko lapansi. 10Iye anali mʼdziko lapansi, ndipo ngakhale kuti dziko lapansi linalengedwa ndi Iye, dziko lapansilo silinamuzindikire Iye. 11Iye anabwera kwa iwo amene anali akeake, koma akewo sanamulandire Iye. 12Koma kwa onse amene anamulandira Iye, kwa amene anakhulupirira mʼdzina lake, Iye anawapatsa mphamvu yokhala ana a Mulungu; 13ana wobadwa osati monga mwachilengedwe, kapena chisankho cha munthu, kapena chifuniro cha mwamuna koma wobadwa mwa Mulungu. 14Mawu anasandulika thupi ndipo anakhala pakati pathu. Ife tinaona ulemerero wake, ulemerero wa Iye amene ndi Mwana mmodzi yekhayo wa Atate, wodzaza ndi chisomo ndi choonadi. 15Yohane achitira umboni za Iye. Iye akufuwula kuti, “Uyu ndi Iye amene ndinati, ‘Iye amene akubwera pambuyo panga ndi wondiposa ine chifukwa, Iyeyo analipo ine ndisanabadwe.’ ” 16Kuchokera mʼkuchuluka kwa chisomo chake ife tonse talandira madalitso pamwamba pa madalitso. 17Pakuti lamulo linapatsidwa kudzera mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinabwera kudzera mwa Yesu Khristu. 18Palibe munthu amene anaona Mulungu, koma Mwana mmodzi yekhayo amene ali wa pamtima pa Atate, ndiye anafotokoza za Iye.




Yesu Ayeretsa Nyumba ya Mulungu

12Zitatha izi Iye anatsikira ku Kaperenawo pamodzi ndi amayi ake, abale ake ndi ophunzira ake. Iwo anakhala kumeneko masiku owerengeka. 13Nthawi ya Paska ya Ayuda itayandikira, Yesu anapita ku Yerusalemu. 14Mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu Iye anapeza anthu akugulitsa ngʼombe, nkhosa ndi nkhunda ndipo ena akusintha ndalama pa matebulo. 15Chifukwa cha zimenezi Iye anapanga chikwapu cha zingwe ndipo anatulutsa onse mʼbwalo la Nyumbayo, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe; Iye anamwaza ndalama zawo ndi kugudubuza matebulo. 16Kwa amene amagulitsa nkhunda, Iye anati, “Tulutsani izi muno! Osasandutsa Nyumba ya Atate anga msika!” 17Ophunzira ake anakumbukira kuti zinalembedwa kuti, “Kudzipereka kwanga ku nyumba yanu kudzandiphetsa.” 18Kenaka Ayuda anamufunsa Yesu kuti, “Kodi mungationetse chizindikiro chodabwitsa chotani chotsimikizira ulamuliro wanu wochitira izi?” 19Yesu anawayankha kuti, “Gwetsani Nyumba ya Mulunguyi ndipo Ine ndidzayimanganso mʼmasiku atatu.” 20Ayuda anayankha kuti, “Zinatenga zaka makumi anayi kumanga Nyumbayi, kodi Inu mungayimange masiku atatu?” 21Koma Nyumba ya Mulungu imene amanena linali thupi lake. 22Iye ataukitsidwa kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira zimene Iye ananena ndipo anakhulupirira Malemba ndi mawu amene Yesu anayankhula. 23Tsopano Iye ali mu Yerusalemu pa phwando la Paska, anthu ambiri anaona zizindikiro zodabwitsa zimene amachita ndipo anakhulupirira dzina lake. 24Koma Yesu sanawakhulupirire iwo, pakuti amadziwa anthu onse. 25Iye sanafune umboni wa wina aliyense popeza amadziwa zomwe zinali mʼmitima mwa anthu.



Yesu Aphunzitsa Nekodimo za Kubadwa Kwatsopano

1Ndipo panali Mfarisi wotchedwa Nekodimo, wa mʼgulu lolamulira la Ayuda. 2Iye anabwera kwa Yesu usiku ndipo anati, “Rabi, ife tikudziwa kuti ndinu aphunzitsi wochokera kwa Mulungu, pakuti palibe amene angachite zizindikiro zodabwitsa zimene Inu mukuchita ngati Mulungu sali naye.” 3Poyankha Yesu ananena kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti, ngati munthu sabadwanso mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu.” 4Nekodimo anati, “Kodi munthu angabadwenso bwanji atakalamba? Kodi angalowe kachiwiri mʼmimba ya amayi ake kuti abadwenso?” 5Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu. 6Thupi limabereka thupi, koma Mzimu amabereka mzimu. 7Iwe usadabwe chifukwa ndakuwuza kuti, ‘Uyenera kubadwanso.’ 8Mphepo imawomba kulikonse kumene ikufuna. Ungathe kumva kuwomba kwake, koma sungathe kudziwa kumene ikuchokera kapena kumene ikupita. Nʼchimodzimodzi ndi amene abadwa ndi Mzimu Woyera.” 9Nekodimo anafunsa kuti, “Kodi izi zingatheke bwanji?” 10Yesu anati, “Iwe mphunzitsi wa Israeli, kodi sukuzindikira zimenezi? 11Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ife tiyankhula zimene tikuzidziwa ndi kuchitira umboni zimene taziona, komabe inu simuvomereza umboni wathu. 12Ine ndikuyankhula kwa iwe zinthu za dziko lapansi ndipo sukukhulupirira. Nanga kodi udzakhulupirira bwanji ngati nditayankhula zinthu zakumwamba? 13Palibe wina aliyense anapita kumwamba, koma yekhayo amene watsika kuchokera kumwamba, Mwana wa Munthu. 14Tsono monga Mose anapachika njoka mʼchipululu, moteronso Mwana wa Munthu ayenera kupachikidwa, 15kuti aliyense amene akhulupirira Iye akhale ndi moyo wosatha. 16“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha. 17Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze, koma kuti akapulumutse dziko lapansi. 18Aliyense wokhulupirira Iye saweruzidwa, koma aliyense wosakhulupirira waweruzidwa kale chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. 19Ndipo chiweruzo ndi ichi: kuwunika kunabwera mʼdziko lapansi, koma anthu anakonda mdima mʼmalo mwa kuwunikako, chifukwa ntchito zawo zinali zoyipa. 20Aliyense wochita zoyipa amadana ndi kuwunika, ndipo sabwera poyera chifukwa cha mantha kuti ntchito zake zingaonekere. 21Koma aliyense wokhala mu choonadi amabwera ku kuwunika, kuti zionekere poyera zimene iye wachita zachitika kudzera mwa Mulungu.”



Yesu Acheza ndi Mayi wa ku Samariya

1Yesu atazindikira kuti Afarisi amva zoti Iye ankapeza ndi kubatiza ophunzira ambiri kupambana Yohane, 2(ngakhale kuti Yesuyo sankabatiza, koma ophunzira ake). 3Iye anachoka ku Yudeya ndi kubwereranso ku Galileya. 4Ndipo Iye anayenera kudutsa mu Samariya. 5Iye anafika mʼmudzi wa Asamariya wotchedwa Sukari, pafupi ndi malo amene Yakobo anapatsa mwana wake Yosefe. 6Chitsime cha Yakobo chinali pamenepo ndipo Yesu atatopa ndi ulendo anakhala pansi pambali pa chitsimecho. Nthawi inali pafupifupi ora lachisanu ndi chimodzi masana. 7Mayi wa Chisamariya atabwera kudzatunga madzi, Yesu anati kwa iye, “Kodi ungandipatse madzi akumwa.” 8(Ophunzira ake nʼkuti atapita mʼmudzi kukagula chakudya). 9Mayiyo anati kwa Iye, “Inu ndinu Myuda ndipo ine ndine Msamariya. Bwanji mukundipempha madzi akumwa?” (Popeza Ayuda ndi Asamariya sankayanjana). 10Yesu anamuyankha kuti, “Koma iwe ukanadziwa mphatso ya Mulungu ndi Iye amene akukupempha madzi akumwa, ukanamupempha ndipo akanakupatsa madzi amoyo.” 11Mayiyo anati, “Ambuye, Inu mulibe kanthu kotungira madzi ndipo chitsime ndi chakuya. Kodi madzi amoyowo mungawatenge kuti? 12Kodi Inu ndinu wamkulu kuposa kholo lathu Yakobo, amene anatipatsa chitsimechi ndipo iye ankamwanso monga anachita ana ake ndi ziweto zake?” 13Yesu anayankha kuti, “Aliyense amene amamwa madzi awa amamvanso ludzu, 14koma aliyense amene adzamwa madzi amene Ine ndidzamupatsa sadzamvanso ludzu. Ndithudi, madzi amene ndidzamupatsa adzakhala kasupe wamadzi wotumphukira ku moyo wosatha.” 15Mayiyo anati kwa Iye, “Ambuye, patseni madzi amenewo kuti ndisadzamvenso ludzu ndi kumabwerabe kuno kudzatunga madzi.” 16Iye anamuwuza kuti, “Pita kayitane mwamuna wako ndipo ubwere naye.” 17Iye anayankha kuti, “Ine ndilibe mwamuna.” Yesu anati kwa iye, “Wakhoza ponena kuti ulibe mwamuna. 18Zoona nʼzakuti iwe wakhala pa banja ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene uli naye tsopano si wako. Zimene wanenazi ndi zoona.” 19Mayiyo anati, “Ambuye, ine ndazindikira kuti Inu ndinu mneneri. 20Makolo athu ankapembedza mʼphiri ili koma inu Ayuda mumati malo amene tiyenera kupembedzera ali ku Yerusalemu.” 21Yesu anati, “Mayi inu khulupirira Ine. Nthawi ikubwera pamene inu simudzapembedza Atate mʼphiri ili kapena mu Yerusalemu. 22Inu Asamariya mumapembedza chimene simukuchidziwa. Ife timapembedza chimene tikuchidziwa, pakuti chipulumutso nʼchochokera kwa Ayuda. 23Koma nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano pamene opembedza woona adzapembedza Atate mu mzimu ndi mʼchoonadi, pakuti opembedza otere ndiwo amene Atate akuwafuna. 24Mulungu ndi Mzimu, ndipo omupembedza Iye ayenera kumupembedza mu mzimu ndi mʼchoonadi.” 25Mayiyo anati, “Ine ndikudziwa kuti Mesiya (wotchedwa Khristu) akubwera. Akabwera, Iye adzafotokoza zonse kwa ife.” 26Ndipo Yesu anamuwuza kuti, “Amene ndikukuyankhulane, ndine amene.”



Yesu Adziwulula kuti ndi Mwana wa Mulungu

16Ndipo popeza Yesu amachita zinthu izi tsiku la Sabata, Ayuda anayamba kumulondalonda. 17Yesu anawawuza kuti, “Atate anga amagwira ntchito nthawi zonse mpaka lero lino, ndipo Inenso ndili pa ntchito.” 18Chifukwa cha ichi Ayuda anawirikiza kufuna kumupha; osati chifukwa chakuswa Sabata kokha komanso chifukwa ankanena kuti Mulungu ndi Atate ake, nadziyesa Iye wofanana ndi Mulungu. 19Yesu anawapatsa yankho ili: “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Mwana sangathe kuchita kanthu pa Iye yekha. Iye amachita zokhazo zimene amaona Atate ake akuchita, chifukwa chilichonse chimene Atate amachita Mwana amachitanso. 20Pakuti Atate amakonda Mwana, amamuonetsa zonse zimene Iwo amachita. Inde, Atate adzamuonetsa zinthu zazikulu kuposa zimenezi ndipo mudzadabwa. 21Pakuti monga Atate amaukitsa akufa nawapatsa moyo, momwemonso Mwana amapereka moyo kwa amene Iye akufuna. 22Komanso, Atate saweruza aliyense koma wapereka kwa Mwana ulamuliro woweruzawo, 23kuti aliyense alemekeze Mwanayo monga momwe amalemekezera Atate. Munthu amene salemekeza Mwana salemekezanso Atate amene anamutuma Mwanayo. 24 “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo. 25Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo. 26Pakuti monga Atate ali gwero la moyo, momwemonso anapereka mphamvu zopereka moyo mwa Mwana. 27Ndipo wamupatsa Iye ulamuliro woweruza chifukwa ndi Mwana wa Munthu. 28 “Musadabwe ndi zimenezi. Pakuti nthawi ikubwera pamene onse amene ali mʼmanda adzamva mawu ake 29ndi kutuluka. Iwo amene anachita zabwino adzauka ndi kupita ku moyo wosatha ndipo amene anachita zoyipa adzauka ndi kupita ku chilango chamuyaya. 30Pakuti sindingathe kuchita kena kalikonse pa ndekha. Ine ndimaweruza molingana ndi zomwe Mulungu wandiwuza ndipo kuweruza kwanga ndi kolungama. Ine sindifuna kudzikondweretsa ndekha koma Iye amene anandituma.



Yesu Chakudya Chamoyo

25Atamupeza mbali ina ya nyanjayo, iwo anamufunsa Iye kuti, “Rabi, mwafika nthawi yanji kuno?” 26Yesu anawayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mukundifuna, osati chifukwa munaona zizindikiro zodabwitsa koma chifukwa munadya chakudya ndi kukhuta. 27Gwirani ntchito, osati chifukwa cha chakudya chimene chimawonongeka koma chifukwa cha chakudya chimene sichiwonongeka mpaka ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani. Mulungu Atate anamusindikiza chizindikiro chomuvomereza.” 28Kenaka anamufunsa Iye kuti, “Kodi tichite chiyani kuti tigwire ntchito za Mulungu?” 29Yesu anayankha kuti, “Ntchito ya Mulungu ndi iyi: Kukhulupirira Iye amene anamutuma.” 30Choncho iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi mudzatipatsa chizindikiro chodabwitsa chotani kuti ife tichione ndi kukhulupirira Inu? Kodi mudzachita chiyani? 31Makolo athu akale anadya mana mʼchipululu; monga zalembedwa: ‘anawapatsa buledi wochokera kumwamba kuti adye.’ ” 32Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti si Mose amene ankakupatsani chakudya chochokera kumwamba, koma ndi Atate anga amene ankakupatsani chakudya chenicheni chochokera kumwamba. 33Pakuti chakudya cha Mulungu ndi Iye amene wabwera kuchokera kumwamba ndi kupereka moyo ku dziko la pansi.” 34Iwo anati, “Ambuye, kuyambira tsopano muzitipatsa buledi ameneyu.” 35Kenaka Yesu ananenetsa kuti, “Ine ndine chakudya chamoyo. Iye amene abwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu. 36Monga ndakuwuzani kale, ngakhale kuti mwandiona simukukhulupirirabe. 37Zonse zimene Atate andipatsa zidzabwera kwa Ine, ndipo aliyense amene adzabwera kwa Ine sindidzamutaya kunja. 38Pakuti Ine ndinatsika kuchokera kumwamba osati kudzachita chifuniro changa koma cha Iye amene anandituma Ine. 39Ndipo chifuniro cha Iye amene anandituma Ine nʼchakuti ndisatayepo ngakhale ndi mmodzi yemwe mwa onse amene Iye wandipatsa, koma kuti ndidzawaukitse kwa akufa pa tsiku lomaliza. 40Pakuti chifuniro cha Atate anga ndi chakuti aliyense amene aona Mwanayo namukhulupirira akhale ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.” 41Pamenepo Ayuda anayamba kungʼungʼudza chifukwa anati, “Ine ndine chakudya chotsika kuchokera kumwamba.” 42Iwo anati, “Kodi uyu si Yesu, mwana wa Yosefe, amene abambo ake ndi amayi ake timawadziwa? Nanga Iyeyu akunena bwanji kuti, ‘Ine ndinatsika kuchokera kumwamba?’ ” 43Yesu anayankha kuti, “Musangʼungʼudze pakati panu.” 44Palibe munthu amene angabwere kwa Ine, ngati Atate amene anandituma Ine samubweretsa. Ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. 45Aneneri analemba kuti, “Onse adzaphunzitsidwa ndi Mulungu! Aliyense amene amamva Atate ndi kuphunzira kwa Iye amabwera kwa Ine. 46Palibe amene anaona Atate koma yekhayo amene achokera kwa Mulungu; yekhayo ndiye anaona Atate. 47Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Iye amene akhulupirira ali nawo moyo wosatha. 48Ine ndine chakudya chamoyo. 49Makolo anu akale anadya mana mʼchipululu, komabe anafa. 50Koma pano pali chakudya chochokera kumwamba, chimene munthu akadya sangafe. 51Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati munthu adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Chakudya chimenechi ndi thupi langa, limene Ine ndidzalipereka kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo.” 52Kenaka Ayuda anayamba kutsutsana kwambiri pakati pawo kuti, “Kodi munthu uyu angathe kutipatsa bwanji thupi lake kuti tidye?” 53Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ngati simungadye thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu. 54Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga ali ndi moyo wosatha ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. 55Pakuti thupi langa ndi chakudya chenicheni ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. 56Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga amakhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye. 57Monga Atate amoyo anandituma Ine, ndipo ndili ndi moyo chifukwa cha Atatewo, chomwechonso amene adya thupi langa adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine. 58Ichi ndiye chakudya chimene chinatsika kuchokera kumwamba. Makolo athu akale anadya mana ndi kufa, koma iye amene adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi yonse.” 59Iye ankanena izi pamene ankaphunzitsa mʼsunagoge mu Kaperenawo.



Za Umboni wa Yesu

12Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, “Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo.” 13Afarisi anamutsutsa Iye nati, “Iwe ukudzichitira umboni wa Iwe mwini, umboni wako siwoona.” 14Yesu anayankha kuti, “Ngakhale Ine ndidzichitire umboni, umboni wangawu ndi woona, pakuti Ine ndikudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita. Koma inu simukudziwa ndi pangʼono pomwe kumene ndinachokera kapena kumene ndikupita. 15Inu mumaweruza potsata maganizo a anthu chabe. Ine sindiweruza munthu wina aliyense. 16Koma Ine ndikati ndiweruze, ndimaweruza molondola, chifukwa Ine sindili ndekha koma ndili ndi Atate amene anandituma. 17Mʼmalamulo anu munalembedwa kuti umboni wa anthu awiri ndi wovomerezeka. 18Ine ndikudzichitira ndekha umboni; ndipo mboni inanso ndi Atate amene anandituma.” 19Kenaka iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi Atate anuwo ali kuti?” Yesu anayankha kuti, “Inu simundidziwa Ine. Atate anganso simuwadziwa. Mukanandidziwa Ine, mukanawadziwanso Atate anga.” 20Iye anayankhula mawu awa pamene amaphunzitsa Nyumba ya Mulungu pafupi ndi malo amene amaponyapo zopereka. Komabe palibe amene anamugwira Iye, chifukwa nthawi yake inali isanakwane.



Yesu Achiritsa Munthu Wosaona Chibadwire

1Iye akuyendabe, anaona munthu wosaona chibadwire. 2Ophunzira ake anamufunsa Iye kuti, “Rabi anachimwa ndani, munthuyu kapena makolo ake, kuti iye abadwe wosaona?” 3Yesu anayankha kuti, “Sikuti iyeyu anachimwa kapena makolo ake, koma izi zinachitika kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iyeyu. 4Ife tiyenera kugwira ntchito za Iye amene anandituma kukanali masana. Usiku ukubwera, pamene wina aliyense sadzagwira ntchito. 5Pamene Ine ndili mʼdziko lapansi, Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi.” 6Atanena izi, Iye anathira malovu pansi ndi kukanda dothi, napaka matopewo mʼmaso a munthuyo. 7Yesu anamuwuza iye kuti, “Pita kasambe mʼdziwe la Siloamu” (mawu awa akutanthauza Wotumidwa). Choncho munthuyo anapita ndi kukasamba ndipo anabwerako akupenya. 8Anzake ndi iwo amene anamuona iye poyamba akupempha anafunsa kuti, “Kodi uyu si munthu amene amapemphapempha uja?” 9Ena ananena kuti anali yemweyo. Ena anati, “Ayi, sakuoneka ngati yemweyo.” Koma iye mwini ananenetsa kuti, “Munthuyo ndine.” 10Iwo anafunsitsa kuti, “Kodi nanga maso ako anatsekuka bwanji?” 11Iye anayankha kuti, “Munthu wina wotchedwa Yesu anakanda dothi ndi kupaka mʼmaso anga. Iye anandiwuza kuti ndipite ku Siloamu ndi kukasamba. Choncho ndinapita kukasamba, ndipo ndikuona.” 12Iwo anamufunsa iye kuti, “Ali kuti munthu ameneyu?” Iye anati, “Ine sindikudziwa.”



Mʼbusa Wabwino ndi Nkhosa Zake

1 “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani inu Afarisi, kuti munthu amene salowera pa khomo mʼkhola la nkhosa, koma amalowera pena pake ndi wakuba ndi wachifwamba. 2Munthu amene amalowera pa khomo ndi mʼbusa wankhosazo. 3Mlonda amamutsekulira khomo, ndipo nkhosa zimamvera mawu ake. Iye amaziyitana mayina nkhosa zakezo, nazitulutsa. 4Akazitulutsa nkhosa zake zonse, iye amazitsogolera, ndipo nkhosa zakezo zimamutsata chifukwa zimadziwa mawu ake. 5Koma nkhosazo sizidzatsatira mlendo. Izo zidzamuthawa chifukwa sizizindikira mawu a mlendo.” 6Yesu ananena mawu ophiphiritsawa, koma Afarisi sanazindikire zimene ankawawuza. 7Choncho Yesu anatinso, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Ine ndine khomo la nkhosa. 8Onse amene anadza ndisanabwere Ine ndi akuba ndi achifwamba, ndipo nkhosa sizinawamvere. 9Ine ndine khomo, aliyense amene alowa kudzera mwa Ine adzapulumuka. Iye adzalowa ndi kutuluka ndi kupeza msipu. 10Mbala sibwera chabe koma kuti idzabe, kupha ndi kuwononga. Ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka. 11 “Ine ndine Mʼbusa wabwino. Mʼbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake. 12Wantchito ndi mʼbusa amene nkhosazo si zake. Choncho, pamene aona mmbulu ukubwera, iye amazisiya nkhosazo ndi kuthawa. Ndipo mmbulu umagwira nkhosazo ndikuzibalalitsa. 13Munthuyo amathawa chifukwa ndi wantchito ndipo sasamalira chilichonse cha nkhosazo. 14 “Ine ndine mʼbusa wabwino. Ine ndimazidziwa nkhosa zanga ndipo nkhosa zangazo zimandidziwa, 15monga momwe Atate amandidziwa Ine, ndiponso Ine kudziwira Atatewo. Ndimapereka moyo wanga chifukwa cha nkhosa. 16Ine ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za gulu ili. Ine ndiyenera kuzibweretsanso. Izonso zidzamvera mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi mʼbusa mmodzi. 17Nʼchifukwa chake Atate anga amandikonda, popeza Ine ndikupereka moyo wanga kuti ndiwutengenso. 18Palibe amene angawuchotse mwa Ine, koma ndikuwupereka mwakufuna kwanga. Ine ndili ndi ulamuliro wa kuwupereka ndi ulamuliro wakuwutenganso. Lamulo ili ndinalandira kwa Atate anga.” 19Pa mawu awa Ayuda anagawikananso. 20Ambiri a iwo anati, “Iye ndi wogwidwa ndi ziwanda ndi wamisala. Chifukwa chiyani mukumvera Iye?” 21Koma ena anati, “Awa si mawu a munthu wogwidwa ndi ziwanda. Kodi ziwanda zingathe bwanji kutsekula maso a wosaona?”



Agriki Afuna Kuona Yesu

20Tsopano panali Agriki ena pakati pa amene anapita kukapembedza ku phwando. 21Iwo anabwera kwa Filipo, wochokera ku Betisaida wa ku Galileya, ndi pempho, nati, “Akulu, ife tikufuna kuona Yesu.” 22Filipo anapita kukawuza Andreya; Andreya ndi Filipo pamodzi anakawuza Yesu. 23Yesu anayankha kuti, “Nthawi yafika yakuti Mwana wa Munthu alemekezedwe. 24Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti, ‘Mbewu ya tirigu imakhala imodzi yokha ngati sikugwa mʼnthaka ndi kufa. Koma ngati imfa, imabereka mbewu zambiri.’ 25Munthu amene amakonda moyo wake adzawutaya, pamene munthu amene amadana ndi moyo wake mʼdziko lino lapansi adzawusungira ku moyo wosatha. 26Aliyense amene atumikira Ine ayenera kunditsata; ndipo kumene Ine ndili, wotumikira wanga adzakhalanso komweko. Atate anga adzalemekeza amene atumikira Ine.



Yesu Aneneratu kuti Petro Adzamukana

31Yudasi atatuluka, Yesu anati, “Tsopano Mwana wa Munthu walemekezedwa, ndipo mwa Iyeyu Mulungu walemekezedwanso. 32Ngati Mulungu walemekezedwa mwa Iye, Mulungu mwini adzalemekezanso Mwana, ndipo amulemekeza nthawi yomweyo. 33 “Ana anga, Ine ndikhala nanu kwa nthawi yochepa chabe. Inu mudzandifunafuna Ine, ndipo monga momwe ndinawawuzira Ayuda, choncho Ine ndikukuwuzani tsopano kuti, kumene Ine ndikupita, inu simungabwereko. 34 “Lamulo latsopano limene ndikukupatsani ndi lakuti: Kondanani wina ndi mnzake, monga momwe Ine ndinakonda inu. Nanunso mukondane wina ndi mnzake. 35Mukamakondana aliyense adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga.” 36Simoni Petro anafunsa kuti, “Ambuye, kodi mukupita kuti?” Yesu anayankha kuti, “Kumene Ine ndikupita iwe sunganditsatire tsopano, koma udzanditsatira mʼtsogolo.” 37Petro anafunsa kuti, “Ambuye, nʼchifukwa chiyani ine sindingakutsatireni tsopano? Ine ndidzapereka moyo wanga chifukwa cha Inu.” 38Kenaka Yesu anayankha kuti, “Kodi iwe udzalolera kutaya moyo chifukwa cha Ine? Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti tambala asanalire, iwe udzandikana katatu!”



Yesu Atonthoza Ophunzira Ake

1 “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu; khulupirirani Inenso. 2Mʼnyumba mwa Atate anga muli zipinda zambiri. Kukanakhala kuti mulibemo ndikanakuwuzani. Ine ndikupita kumeneko kukakukonzerani malo. 3Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti kumene kuli Ineko, inunso mukakhale komweko. 4Inu mukudziwa njira ya kumene Ine ndikupita.” 5Tomasi anati kwa Iye, “Ambuye ife sitikudziwa kumene Inu mukupita, nanga tingadziwe bwanji njirayo?” 6Yesu anayankha kuti, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine. 7Mukanandidziwadi Ine, mukanadziwanso Atate anga. Kuyambira tsopano, mukuwadziwa ndipo mwawaona.” 8Filipo anati, “Ambuye, tionetseni Atatewo ndipo ife tikhutitsidwa.” 9Yesu anayankha kuti, “Kodi iwe Filipo, ndakhala pakati panu nthawi yonseyi ndipo iwe sukundidziwabe? Aliyense amene waona Ine, waonanso Atate. Tsono ukunena bwanji kuti, ‘Tionetseni Atate?’ 10Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndili mwa Atate, ndipo Atate ali mwa Ine? Mawu amene Ine ndiyankhula kwa inu si mawu anga okha koma ndi mawu Atate wokhala mwa Ine, amene akugwira ntchito yake. 11Khulupirirani Ine pamene ndi kuti Ine ndili mwa Atate ndipo Atate ali mwa Ine. Koma ngati si chomwecho, khulupiriranitu Ine chifukwa cha ntchito zanga zodabwitsa. 12Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene akhulupirira Ine adzachita zimene Ine ndakhala ndikuchita. Iye adzachita ngakhale zinthu zazikulu kuposa zimenezi, chifukwa ndikupita kwa Atate. 13Ndipo Ine ndidzachita chilichonse chimene inu mudzapempha mʼdzina langa kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana. 14Ngati mudzapempha kanthu kalikonse mʼdzina langa, Ine ndidzachita.

Yesu Njira ya kwa Atate

15 “Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga. 16Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse. 17Nkhosweyo ndiye Mzimu wachoonadi. Dziko lapansi silingalandire Nkhosweyi chifukwa samuona kapena kumudziwa. Koma inu mumamudziwa pakuti amakhala nanu ndipo adzakhala mwa inu. 18Ine sindikusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ine ndidzabweranso kwa inu. 19Patsala nthawi yochepa dziko lapansi silidzandionanso koma inu mudzandiona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo. 20Tsiku limenelo inu mudzazindikira kuti Ine ndili mwa Atate, ndipo inu muli mwa Ine, ndipo Ine ndili mwa inu. 21Iye amene amadziwa malamulo anga ndi kuwasunga ndiye amene amandikonda. Wokonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga ndipo Inenso ndidzamukonda ndikudzionetsa ndekha kwa iye.” 22Kenaka Yudasi (osati Yudasi Isikarioti) anati, “Koma Ambuye, nʼchifukwa chiyani mukufuna kudzionetsa nokha kwa ife, osati ku dziko lapansi?” 23Yesu anamuyankha kuti, “Ngati wina aliyense andikonda Ine, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera ndi kukhala naye. 24Iye amene sandikonda Ine sasunga mawu anga. Mawu awa amene mukumva si anga ndi a Atate amene anandituma Ine. 25 “Ndayankhula zonsezi ndikanali nanu. 26Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamutumiza mʼdzina langa adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndinakuwuzani. 27Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha. 28 “Inu munamva Ine ndikunena kuti, ‘Ine ndikupita ndipo ndidzabweranso kwa inu.’ Mukanandikonda, mukanasangalala kuti Ine ndikupita kwa Atate, pakuti Atate ndi wamkulu kuposa Ine. 29Ine ndakuwuzani tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika mudzakhulupirire. 30Ine sindiyankhulanso nanu zambiri nthawi yayitali popeza wolamulira dziko lapansi akubwera. Iye alibe mphamvu pa Ine, 31koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti Ine ndimakonda Atate ndi kuti ndimachita zokhazokha zimene Atate wandilamulira Ine. “Nyamukani; tizipita.”



Mpesa ndi Nthambi

1 “Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate anga ndiye mwini munda. 2Iye amadula nthambi iliyonse ya mwa Ine imene sibala chipatso, koma nthambi iliyonse imene imabala chipatso amayisadzira bwino kuti ibale zipatso zambiri. 3Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ndayankhula inu. 4Khalani mwa Ine, monga Ine ndili mwa inu. Palibe nthambi imene ingabereke chipatso pa yokha ngati sinalumikizike ku mpesa. Chomwechonso inu simungathe kubereka chipatso pokhapokha mutakhala mwa Ine. 5 “Ine ndine mpesa; inu ndinu nthambi zake. Ngati munthu akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye, adzabereka zipatso zambiri; popanda Ine simungathe kuchita kanthu. 6Ngati wina aliyense sakhala mwa Ine, iyeyo ali ngati nthambi imene yatayidwa ndi kufota. Nthambi zotero zimatoledwa, kuponyedwa pa moto ndi kupsa. 7Ngati inu mukhala mwa Ine ndipo mawu anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene mukufuna ndipo mudzapatsidwa. 8Atate anga amalemekezedwa mukamabereka zipatso zochuluka, ndipo potero mudzionetsa kuti ndinu ophunzira anga. 9 “Monga momwe Atate amandikondera Ine, Inenso ndakukondani. Tsopano khalani mʼchikondi changa. 10Ngati mumvera malamulo anga, mudzakhala mʼchikondi changa, monga Ine ndimamvera malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala mʼchikondi chawo. 11Ine ndakuwuzani izi kuti chimwemwe changa chikhale mwa Inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chokwanira. 12Lamulo langa ndi ili: ‘Kondanani wina ndi mnzake monga Ine ndakonda inu.’ 13Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. 14Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene Ine ndikulamulani. 15Ine sindikutchulaninso antchito, chifukwa wantchito sadziwa zimene bwana wake akuchita. Mʼmalo mwake Ine ndakutchani abwenzi pakuti zilizonse zimene ndinaphunzira kwa Atate, Ine ndakudziwitsani. 16Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani kuti mupite ndi kukabereka zipatso, zipatso zake za nthawi yayitali. Choncho Atate adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. 17Lamulo langa ndi ili: ‘Muzikondana.’



Yesu Adzipempherera Yekha, Ophunzira Ake, Okhulupirira Onse

1Yesu atatha kunena izi, anayangʼana kumwamba ndipo anapemphera: “Atate, nthawi yafika. Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanuyo akulemekezeni Inu. 2Pakuti Inu munamupatsa Iye ulamuliro pa anthu onse kuti apereke moyo wosatha kwa onse amene mwamupatsa. 3Tsono moyo wosathawo ndi uwu: Iwo akudziweni Inu, Mulungu yekhayo woona, ndi Yesu Khristu, amene Inu mwamutuma. 4Ine ndabweretsa ulemerero wanu pa dziko pamene ndamaliza ntchito imene munandipatsa kuti ndi igwire. 5Ndipo tsopano, Atate, ndilemekezeni Ine pamaso panu ndi ulemerero uja umene ndinali nawo kwa Inu dziko lapansi lisanayambe. 6 “Ine ndawadziwitsa za Inu anthu amene munandipatsa mʼdziko lapansi. Iwo anali anu. Inu munawapereka kwa Ine ndipo amvera mawu anu. 7Tsopano akudziwa kuti zonse zimene munandipatsa nʼzochokera kwa Inu. 8Pakuti Ine ndiwapatsa mawu amene Inu munandipatsa ndipo awalandira. Iwo akudziwa ndithu kuti Ine ndinachokera kwa Inu, ndipo akukhulupirira kuti Inu ndiye amene munandituma Ine. 9Ine ndikuwapempherera. Ine sindikupempherera dziko lapansi, koma anthu amene Inu mwandipatsa, pakuti ndi anu. 10Zonse zimene Ine ndili nazo ndi zanu, ndipo zonse zimene Inu muli nazo ndi zanga. Choncho Ine ndalemekezedwa mwa iwowo. 11Ine sindikukhalanso mʼdziko lapansi nthawi yayitali, koma iwo akanali mʼdziko lapansi. Ine ndikubwera kwa Inu. Atate Woyera, atetezeni ndi mphamvu za dzina lanu. Dzina limene munandipatsa Ine, kuti iwo akhale amodzi monga Ife tili amodzi. 12Pamene ndinali nawo, ndinawateteza ndi kuwasunga mosamala mʼdzina limene munandipatsa. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatayika kupatula yekhayo amene anayenera kuwonongeka kuti malemba akwaniritsidwe. 13 “Tsopano ndikubwera kwa Inu. Ndikunena izi ndikanali mʼdziko lapansi, kuti iwo akhale ndi muyeso wodzaza wachimwemwe changa mʼkati mwawo. 14Ine ndawapatsa mawu anu ndipo dziko lapansi likudana nawo, pakuti sali a dziko lapansi monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. 15Sindikupempha kuti muwachotse mʼdziko lapansi koma kuti muwateteze kwa woyipayo. 16Iwo si a dziko lapansi, monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. 17Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi. 18Monga Inu munandituma Ine mʼdziko lapansi, Inenso ndikuwatuma mʼdziko lapansi. 19Chifukwa cha iwowa Ine ndikudziyeretsa, kuti iwo ayeretsedwenso kwenikweni. 20 “Ine sindikupempherera iwo okhawa, komanso amene adzandikhulupirira chifukwa cha uthenga wawo. 21Ndikuwapempherera kuti onsewa akhale amodzi. Monga Inu Atate muli mwa Ine ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife kuti dziko lapansi likhulupirire kuti Inu munandituma Ine. 22Ine ndawapatsa ulemerero umene munandipatsa Ine, kuti akhale amodzi monga Ife tili amodzi. 23Ine ndikhale mwa iwo ndipo Inu mwa Ine kuti umodzi wawo ukhale wangwiro. Choncho dziko lapansi lidzadziwa kuti Inu munandituma Ine ndipo Inu mwawakonda iwowa monga momwe Inu munandikondera Ine. 24 “Atate, Ine ndikufuna kuti anthu amene mwandipatsa Ine adzakhale ndi Ine kumene kuli Ine, ndi kuona ulemerero wanga, ulemerero umene munandipatsa chifukwa Inu munandikonda dziko lapansi lisanalengedwe. 25 “Atate wolungama, ngakhale kuti dziko lapansi silikudziwani Inu, Ine ndimakudziwani, ndipo iwo amadziwa kuti Inu munandituma Ine. 26Ine ndawadziwitsa dzina lanu, ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzina lanulo, kuti chikondi chomwe munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndipo Ine mwa iwo.”



Imfa ya Yesu

28Atadziwa kuti zonse zatha tsopano komanso kuti malemba akwaniritsidwe, Yesu anati, “Ine ndili ndi ludzu.” 29Pomwepo panali mtsuko wodzaza ndi vinyo wosasa, choncho iwo ananyika chinkhupule ndi kuchisomeka ku mtengo wa hisope nachifikitsa kukamwa kwa Yesu. 30Yesu atalandira chakumwachi anati, “Kwatha.” Ndipo Iye anaweramitsa mutu wake napereka mzimu wake. 31Popeza linali Tsiku Lokonzekera ndipo tsiku linalo linali Sabata lapadera; Ayuda sanafune kuti mitembo ikhale pa mtanda pa Sabata, iwo anapempha Pilato kuti akathyole miyendo ndi kutsitsa mitemboyo. 32Chifukwa chake asilikali anabwera ndi kuthyola miyendo ya munthu oyamba amene anapachikidwa ndi Yesu ndipo kenaka ya winayo. 33Koma atafika pa Yesu ndi kupeza kuti anali atamwalira kale, iwo sanathyole miyendo yake. 34Mʼmalo mwake, mmodzi wa asilikaliwo anamubaya Yesu ndi mkondo mʼnthiti, ndipo nthawi yomweyo munatuluka magazi ndi madzi. 35Munthu amene anaona izi wapereka umboni ndipo umboni wake ndi woona. Iye akudziwa kuti akunena choonadi kuti inunso mukhulupirire. 36Zinthu izi zinachitika kuti malemba akwaniritsidwe: “Palibe limodzi la mafupa limene lidzathyoledwa,” 37ndi monga lemba linanso linena, “Iwo adzayangʼana Iye amene iwo anamubaya.”



Yesu Aonekera kwa Ophunzira ake Tomasi Palibe

19Madzulo a tsiku limenelo limene linali loyamba la Sabata ophunzira ake ali pamodzi, atatseka ndi kukhoma zitseko chifukwa choopa Ayuda, Yesu anabwera ndi kuyima pakati pawo nati, “Mtendere ukhale nanu!” 20Iye atatha kunena izi, anawaonetsa manja ake ndi mʼnthiti mwake. Ophunzira anasangalala kwambiri pamene anaona Ambuye. 21Yesu anatinso, “Mtendere ukhale nanu! Monga Atate anandituma Ine, Inenso ndikukutumani.” 22Ndi mawu amenewo Iye anawapumira ndipo anati, “Landirani Mzimu Woyera. 23Ngati mukhululukira aliyense machimo ake, iwo akhululukidwa; ngati simuwakhululukira, iwo sanakhululukidwe.”