Lembani dzina lanu loyamba:

Tiyeni tiyambepo {{ personName }}

…uthenga omwe mwakhala mukuuyembekezera

Pa tsamba iri mupezapo mayankho ambiri a mafunso a moyo wanu. Mafunso monga, "Kodi cholinga changa pa dziko ndi chani?' "Bwanji ndikukhala ngati ndilibe mtendere umene anthu ena ali nao?" kapena, "Moyo basi ndi choncho basi?" Tsambali likuululirani mayankho a mafunso awa komanso ena ambiri. Mwina simungathe inu kuzindikira, koma muli olekanitsidwa ndi Mulengi wanu Mulungu. Ndinu olekanitsidwa mwa chibadwidwe chanu. Uthenga wathu kwa inu ndi wa chiyembekezo chifukwa Mulungu amakukondani ndipo ndi khumbo lake kuti muyanjane naye ndipo wapereka njira yoti mubwerere kwa iye. Njira yomwe Mulungu waperekayi ndi yoonetsetsa kuti kulekanitsidwa kwanu ndi Mulungu kusakhale kwa muyaya.

{{ personName }}, kodi mukadakonda kudziwa za njirayi?

Kodi mukufuka:

  • -kudziwa za cholinga cha moyo wanu?
  • - kuti mupeze chimwemwe komanso kupeputsidwa komwe kumadza ndi kukhululukidwa kwa zolakwa zomwe munachita kumbuyoku?
  • -kuti mukhale ndi kutsimikizidwa mtima podziwa kuti moyo si pansi pokha pano koma chiyemnekezo cha moyo wosatha kukwamba?

Chifungulo: Chikhulupiriro ndicho chifungulu chomwe chimatsegula makomo a zinthu zambiri.

Ndi chikondi cha Mulungu ku "dziko la pansi", anthu ngati ine ndi inu {{ personName }}, chomwe chinampangitsa Mulungu kupereka njira kuti muthe kupeza nawo chikondi ndi mtendere zomwe zimadza ukayanjanitsidwa Naye. Mulungu akufuna moyo wanu kuti ukhale wodzadzidwa ndi mtendere komanso chimwemwe ndi anthu ena komanso ndi Iye ngakhale pomwe mukudutsa mu nyengo zowawitsa.

Pakuti Mulungu anakonda {{ personName }} kotero kuti anapatsa mwana wake wobadwa yekha, kuti {{ personName }} akakhulupirira Iye asatayike koma khale nao moyo wosatha.

Mau a mu Baibulo pa Yohane 3:16

Pezani ma pulani a Mulungu: Mtendere ndi Moyo

Ndi cholinga cha Mulungu kuti inu mukhale ndi moyo wochuluka padziko pano. Nanga bwanji anthu ambiri sakutha kukhala nao moyo wochulukawu? Yohane 10:10

stap1

Vuto: Pali kulekana pakati pa Mulungu ndi {{ personName }}

Tchimo lakulekanitsani inuyo ndi Mulungu. Zoona, mkono wa Ambuye si waufupi kuti siungapulumutse, kapena khutu lake silogontha. Koma machimo anu akulekanitsani ndi Mulungu; machimo anu abisa nkhope yake kwa inu, kotero kuti sangamve. Yesaya 59:1-2. Izi zadzetsa kulekana pakati pa inu ndi Mulungu. {{ personName }}, inuyo munabadwa ochimwa kamba ka tchimo la Adamu komanso mumachimwa mwa kusankha. Choncho pali kulekana kumeneku pakati pa inuyo ndi Mulungu.

{{ personName }}

Mulungu

stap2

Mulungu analenga anthu muchifanizo chake kuti tikakhale pa chiyanjano chokoma ndi Mulungu wathu chomwe chingapereke ulemerero kwa Iye, kuti tikakhale pa ubwenzi ndi Mulungu. Mulungu analenga dziko lokongola kuti ife tikasangalalemo ndi kunthunthumira ndi chilengedwe chake. Anatipatsa ife mwayi wa moyo wodabwitsa komanso wokwaniritsidwa.

{{ personName }}, Mulungu sanalenge chidole koma munthu muchifanizo chake, yemwe ali ndi mwayi wa kusankha kumukonda komanso kumumvera Mulungu ndikusangalala naye ndi zonse zomwe anamukonzera munthuyo. Chifukwa cha mwayi wa kusankha, munthu ali ndi kuthekera kosankha kusamumvera Mulungu komanso kusamukonda. Kuti munthu ukhale ndi ubwenzi wabwino, chikondi choona payenera kukhala chisankho.Tsinde la chikondi sikukakamizidwa ngati ndiwe chidole ayi koma kusankha.

Komano, munthu woyamba kulengedwa anasankha njira yake ya kusamverra yomwe imatchedwa kuti tchimo. Tchimo limatanthauza kuti kuphonya pomwe walinga, chifukwa Mulungu anali ndi cholinga chabwino cha ife. Choncho chilango cha tchimo sikuti chinali cha munthu woyamba yekha Adamu ndi mkazi woyamba Hava ayi, koma anthu onse popeza tchimolo linasefukira ku mtundu wonse wa anthu.

Baibulo likuti:

"Chifukwa chake monga uchimo unalowa m'dzikolapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa. Aroma 5:12

pophonya pomwe walinga, zimapangitsa kulekana ndi Mulungu komanso ubale unasokonekera. Chotsatira chake ndi kulekanako ndipo palibe mlatho omwe ungalumikize. Ngakhale titha pa tokha kuyesera ndi njira izi:

  • Miyambo ya chipembedzo
  • Kukhala moyo wabwino
  • Kusinkhasinkha
  • ntchito za chifundo
  • moyo wolowa mmanja
stap3

Ndi njira zina zambiri koma palibe njira iriyonse yomwe ingatilumikize popeza Mulungu ndi woyera koma osati ife. Ngakhale tingayesetse ndi zomwe timapanga sitingathe kudzichotsera tchimo kuti tisaphonye cholinga chake.

Baibulo limati: "pakuti onse anachimwa naperewera pa ulemerero wa Yehova". Aroma 3:23

"Pakuti mphoto ya uchimo ndi imfa, koma mphatso ya Mulungu ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye wathu." Aroma 6:23

Pali yankho limodzi lokha la vuto limeneri

Yankho la Mulungu: Yesu Khristu

{{ personName }}

Mulungu

stap4

Yesu Khristu

Mulungu anadziwa kuti iye yekha ndi amene anayenera kupereka yankho la tchimo limene linatilekanitsa ndi Iye. Yankholi linatanthauza kuti Mulungu abwere kwa ife ngati munthu, kudzera mwa Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu.Yesu amene akanakwanitsa chomwe wina aliyense sakanatha. Anakhala moyo wopanda tchimo womwe Mulungu anafuna ndipo Iye anadzipereka kusinthitsa moyo wake ndi wathu podzitengera chilango chathu kaamba ka tchimo mmalo mwa ife.

Mu chiyanjano ndi anthu ena, mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Khristu Yesu:

amene pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanachiyese cholanda kukhala wofana ndi Mulungu, koma anadzikhutula yekha natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m'mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa mmaonekedwea munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pa mtanda. Afilipi 2:5-8

Potifera kaamba ka machimo athu, Yesu Khristu analumikiza phompho limene linali pakati pa Mulungu ndi ife.

Baibulo likuti:

"Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha mmenemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khrustu adatifera ife." Aroma 5:8

Ndipo Yesu ananena motere: Yesu anayankha naye, "Ine ndine Njira, ndi Choonadi, ndi Moyo; palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine." Yohane 14:6

Pomaliza, Mulungu yekha wabwera ndi yankho. Mulungu anasanduka Munthu ndipo mwa Munthuyo, Yesu Khristu, ndipo anachotsa mlekano umene unalipo pakati pa Mulungu ndi ife. Nchifukwa chake anabwera pa dziko la pansi, anafa imfa yowawa pa mtanda natinyamulira chilango cha machimo athu.

Baibulo likuti:

Koma Mulungu atsimikiza chikondi chake cha mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife. Aroma5:8

Pa nthawi inanso:

Yesu anayankha nati, "Ine ndine Njira, ndi Choonadi, ndi Moyo; palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine."

{{ personName }}

Mulungu

  • kusasangalala
  • kulekanitsidwa
  • kutsutsika mtima
  • kusatsimikizika
  • kusowa cholinga
  • mavuto ndi nkhawa
  • chisangalalo
  • chiyanjano ndi ubale
  • chikhululukiro
  • moyo wosatha
  • moyo wochuluka
  • mtendere
stap5

Yesu Khristu

{{ personName }}, monga mukuona, aliyense mdziko la pansi anabadwa wolekanitsidwa ndi Mulungu kaamba ka tchimo. {{ personName }}, inuyo, ndi wina aliyense anapezeka olakwa ndipo ali pansi pa chiweruzo chamuyaya. Mulungu sakukufunirani inuyo ndi wina aliyense izi, wakulezerani mtima, posafuna kuti inu ndi wina aliyense akatayike koma kuti aliyense alape napeza moyo wosatha. Ngati simuchitapo kanthu ndiye kuti mukhalabe olekana ndi Mulungu. Mulungu akukuitanani pano kuti musankhe moyo; Iye akukupatsani inu mwayi kuti musanduke mwana wake ndipo iye atate wanu. Simumalungamitsidwa ndi Mulungu kapena machimo anu kukhululukidwa chifukwa cha zochitika mchipembedzo monga ubatizo kapena kuvomerezedwa ngakhalenso kutsatira za chilamulo cha chipembedzo ngakhalenso kuchita ntchito zabwino. kusankha Yesu ndiko kusankha Mulungu, ichi ndicho chikhulupiriro chodza mwa chisomo cha Mulungu. palibe chisankho china choposa chomwe inu mungapange choposa ichi. Mumasanduka kukhala mwana wa Mulungu pokhulupirira kuti iye mmene aliri komanso ndi uthenga wake.

Baibulo likuti:

Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu. Yohane 1:12

Baibulo limatitsimikizira kukhulupirira uthenga wa Mulungu ndi choona cha chimene Iye ali ndizomwe Iye wachita ndi moyo wake, imfa yake ndi kuukanso kwake kwa akufa.

Baibulo likuti:

Ngati udzavomereze m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka: pakuti ndi mtima akhulupirira kutengapo chilungamo; ndi mkamwa avomereza kutengapo chipulumutso. Aroma 10:9-10

Mukatero mumalandira chikhululukiro cha machimo. Pano ndinu olungamitsidwa mwa chikhulupiriro ndipo muli ndi tendere ndi Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu. Uku ndiko "kukhala ndi chikhulupiriro". Kutanthauza 'kumukhulupirira Yesu'. {{ personName }}, mukuyenera kupanga izi panokha, kulandira uthenga Wake ndipo choona ichi ndi kumulandira Yesu. Kotero Yesu akhala Mbuye wa moyo wanu.

{{ personName }}, inu musankha chiyani?

stap6

Baibulo likuti:

Koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwo anapasa mphamvu yakukhala ana Mulungu. (Yohane 1:12)

{{ personName }}, kodi inu:

1. mukuzindikira kuti ndinu ochimwa ndi olekanitsidwa ndi Mulungu?

2. mukukhulupirira kuti mukuyenera kum'khulupirira Yesu Khristu kuti muyanjane ndi Mulungu?

3. mumupempha Yesu kuti akukhululukireni popeza anasenza kale chilango chanu?

4. mukukhulupirira kuti Iye ndi Mbuye ndipo anauka kwa akufa?

{{ personName }}, ngati mwayankha eya ku mafunsowa, muuzeni Mulungu mu pemphero chifukwa akudziwa kale za mu mtima mwanu.

Pano mutha kumuyamika Mulungu kuti machimo anu akhululukidwa kaamba ka mwazi ndi nsembe ya Yesu.

5. pano ndi nthawi yomuuza Mulungu kuti mukufuna kumutsatira Iye moyo wanu wonse chifukwa Baibuo likuti pano ndinu "Olengedwa Watsopano". 2 Akorinto 5"16-17

Popemphera kwa Mulungu mutha kunena chonchi:

Ambuye Mulungu ndaona kuti ndine ochimwa ndipo ndikufunika chikhululukiro chanu. Ndazindikira kuti Yesu Khristu anandifera ine ndipo anauka wa akufa. Ndiri okonzeka kusiya ntchito zanga zakale ndi kuti ndikudziweni Inu Atate wanga ndi kuti ndikudziweni bwinobwino. Ndi thandizo lanu, ndiri okonzeka kukutsatirani Inu ngati Mbuye wa moyo wanga komanso ndikukumverani Inu. Amen